ayisha cover art

생성일: 3월 23, 2026

가사

[intro]
Mmmmmm ndine ALEX BITON.

[Vers1]
Dzina langa ndine Alex biton.ndimagwila ntchito ya bening'i. eya zimavuta koma nthawi Zina zimayenda kuyesesa kuti ndisakhale opempha.kwacha mmamawa mwanthawi zonse.ndatsegula shopu inu mwanthawi zonse ndayika nyimbo ndamaliza voliyomu yonse koma osadziwa imfa inkangozembela pang'ono pang'ono inkangosendela poshakhalisa nkhani yachisoni inafika akuti mwana wakwathu ayisha wamwalila chisoni chinandigwela pompo ndinayamba kulila.

[Corus]
Ayisha!!!!! ayisha ,ayisha analakwa chani?ndili ndi mafunso ochuluka .imfa Kodi ndichifukwa chani watenga mwana osalakwa?pano ndikulila mm'bale wanga ndimasangalala ndikamuwona ndichifukwa chani watenga chimwemwe changa yiiiiiii!!!! mayoooo!!!!! Ayisha wasiya aliyense akulila.

[Vers2]
Koma imfa ukanakakhala munthu ndikulumbila walayiii mkanakupha kutenga mwana osalakwa mkulakwa.ntengo umamela ndimizu ndikukula mosangalala koma ukagwa mizu imatsala ndikuphuka koma iwe imfa ukuyamba mizu pamenepo waganiza bwanji ukutenga mwana mang'ono chifukwa chani ooooo watisiya muchisoni watisiya tikulila .