amayi cover art

Создано янв 11, 2026

Тексты

Nabola kale lija
‎Nabola ndikukhala Ndekha muja!!
‎Ndinkakhala mosangalala
‎Koma ndimene ndinalowa Banjamu
‎Ndinaziputila Mavuto!!
‎Oh ine!!!
‎Amayo oh ine!!
‎Nyumba kumalipila Ndekha
‎Anah Fizi kumalipila Ndekha
‎Chakudya kumagula Ndekha
‎Ndalama mumazipeza
‎Koma komwe zimapita
‎sikumadziwika!!



‎(chorus)

‎Anthu akamati zikundiyendela
‎Ndimangoti zowonadi zikuyenda
‎Chosecho pasi pamtima ndikuva kuwawa
‎Ena amati Banja landiyanja
‎Mamuna akundisamala
‎Osadziwa kuti ndine ndikumusamala
‎Anandipeza ndili ndi Anah awili
‎Analonjeza kuti azawasamala
‎Koma lelo ndikudabwa kuti Kodi
‎Ndapezaso Mwana wina wa Chitatu
‎Chifukwatu chili chose Ndinapanga Ndekha pa Nkhomo
‎Anah sanawagulileko Olo chovala
‎Ndiye mwina Amwali mukudabwa
‎Kuti bwanji sindikubwelela wina Mwana
‎Ine ndimazifuda kuti ngati akukanika kuveka olo kudyetsa Anawa
‎Ndiye azandipatse Mwana wake eeeh
‎Ine ndizavutika ndizavutika ndisaname


‎(verse)

‎Azanga Azanga!
‎Ndithandizeni!!
‎Ndinalifuna Banja ine oh
‎Ndithandizeni!!
‎Ndipange naye bwanji Mamunayi!!
‎Abale ndithandizeni
‎Kapena mwina ndipilile ine!!
‎Oh Abale ndithandizeni!!
‎Nabola paja poyamba paja
‎Zinali bwino(ndikukhala Ndekha)
‎Amayi kuno ndikulila muntima
‎Misozi yosatha
‎Chikondi chake Mamunayi ndichabodza
‎Anabwela ndi nkhope ya Chikondi
‎Osadziwa kuti ndi nkhalamo
‎Ichi ndi chindele
‎Amayi uyu ndi Ntchewe
‎Ndili pamoto ine
‎Amayi uyu ndi Chibwatiko Cha Mamuna


‎(chorus)

‎Banja lanji ili Bambo
‎Lokhalila kukudandawulani
‎Nkhalidwe lanu loyipa
‎Munayamba kuliwonetsa ndi kale
‎Ndinkati mwina muzasitha
‎Koma apa, aah zanyanya!!
‎Ndili pa Banja koma
‎Ndine Batchala!!
‎Chimamuna ichi ndi Chi Mfiti!!
‎Ndalama zanga akufuna kundiwonongela!!
‎Ndikafusa amakalipa penaso kundimenya!!
‎Amanditenga ngati ine Ng'ombe yake
‎Yongomulimila ndalama iye ndikumakolala!!